5. Ndipo anamuuza iye, M'Betelehemu wa Yudeya; cifukwa kunalembedwa kotere ndi mneneri, kuti,
6. Ndipo iwe: Betelehemu, dziko la Yudeya,Sukhala konse wamng'onong'ono mwa akuru a Yudeya.Pakuti Wotsogolera adzacokera mwaiwe,Amene adzaweta anthu anga Aisrayeli.
7. Pomwepo Herode anawaitana Anzeruwo m'tseri, nafunsitsa iwo nthawi yace idaoneka nyenyeziyo.
8. Nawatumiza ku Betelehemu, nati, Yendani mufunitsitse za kamwanako; ndipo pamene mudzampeza, mundibwezere mau, kuti inenso ndidzadze kudzamlambira Iye.
9. Ndipo iwo, m'mene anamva mfumu, anamuka; ndipo onani, nyenyezi ija anaiona kum'mawa, inawatsogolera iwo, kufikira inadza niima pamwamba pomwe panali kamwanako.
10. Ndipo iwo poona nyenyeziyo, anakondwera ndi kukondwera kwakukuru.
11. Ndipo pofika ku nyumba anaona kamwanako ndi Mariya amace, ndipo anagwa pansi namgwadira Iye; namasula cuma cao, nampatsa Iye mitulo, ndiyo golidi ndi libano ndi mure.
12. Ndipo iwo, pocenjezedwa m'kulota kuti asabwerere kwa Herode, anacoka kupita ku dziko lao pa njira yina.
13. Ndipo pamene iwo anacoka, onani, mngelo wa Ambuye anaonekera kwa Yosefe m'kulota, nati, Tauka, nutenge kamwanako ndi amace, nuthawire ku Aigupto, nukakhale kumeneko kufikira ndidzakuuza iwe; pakuti Herode adzafuna kamwana kukaononga Iko.
14. Ndipo iye ananyamuka natenga kamwana ndi amace usiku, nacoka kupita ku Aigupto;
15. nakhalabe kumeneko kufikira atamwalira Herode; kuti cikacitidwe conenedwa ndi Ambuye mwa mneneri kuti,Ndinaitana Mwana wanga aturuke m'Aigupto.
16. Pamenepo Herode, poona kuti anampusitsa Anzeruwo, anapsa mtima ndithu, natumiza ena kukaononga tiana tonse ta m'Betelehemu ndi ta m'miraga yace yonse, takufikira zaka ziwiri ndi tating'ono tonse, monga mwa nthawi imeneyo iye anafunsitsa kwa Anzeruwo.
17. Pomwepo cinacitidwa conenedwa ndi Yeremiya mneneri, kuti,
18. Mau anamveka m'Rama,Maliro ndi kucema kwambiri;Rakele wolira ana ace,Wosafuna kusangalatsidwa,Cifukwa palibe iwo.