Mateyu 17:1-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo atapita masiku asanu ndi limodzi, Yesu anatenga Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane mbale wace, napita nao pa okha pa phiri lalitari;

2. ndipo Iye anasandulika pamaso pao; ndipo nkhope yace inawala monga dzuwa, ndi zobvala zace zinakhala zoyera mbu monga kuwala.

3. Ndipo onani, Mose ndi Eliya anaonekera kwa iwo, alinkulankhula ndi Iye.

4. Ndipo Petro anayankha, nati kwa Yesu, Ambuye, kuli bwino kuti ife tikhale pano; ngati mulola ndidzamanga pane misasa itatu; umodzi wa Inu, ndi wina wa Mose, ndi wina wa Eliya.

5. Akali cilankhulire, onani, mtambo wowala unawaphi mba iwo: ndipo onani, mau alikunena mumtambo, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera, mverani Iye.

6. Ndipo pamene ophunzira anamva, anagwa nkhope zao pansi, naopa kwakukuru.

7. Ndipo Yesu anadza, nawakhudza nati, Ukani, musaopa,

8. Ndipo iwo, pokweza maso ao sanaona munthu, koma Yesu yekha.

9. Ndipo pamene anali kutsika paphiri, Yesu anawalangiza iwo kuti, Musakauze munthu coonekaco, kufikira Mwana wa munthu adadzauka kwa akufa.

10. Ndipo ophunzira ace anamfunsa, nanena, Ndipo bwanji alembi amanena kuti Eliya ndiye atsogole kudza?

11. Ndipo Iye anayankha, nati, Eliya akudzatu, nadzabwezera zinthu zonse;

12. koma ndinena kwa inu, kuti Eliya anadza kale, ndipo iwo sanamdziwa iye, koma anamcitira zonse zimene anazifuna iwo. Ndipo conconso Mwana wa munthu adzazunzidwa ndi iwo.

13. Pomwepo ophunzira anazindikira kuti analankhula nao za Yohane Mbatizi.

Mateyu 17