38. ndipo munda ndiwo dziko lapansi; ndi mbeu yabwino ndiyo ana a Ufumuwo; ndi namsongole ndiye ana a woipayo;
39. ndipo mdani amene anamfesa uwu ndiye mdierekezi: ndi kututa ndico cimariziro ca nthawi ya pansi pano; ndi otutawo ndiwo angelo.
40. Ndipo monga namsongole asonkhanitsidwa pamodzi, natenthedwa pamoto, matero mudzakhala m'cimariziro ca nthawi ya pansi pano.
41. Mwana wa munthu adzatuma angelo ace, ndipo iwo adzasonkhanitsa pamodzi, ndi kucotsa mu Ufumu wace zokhumudwitsa zonse, ndi anthu akucita kusayeruzika,
42. ndipo adzawataya iwo m'ng'anjo yamoto; kumeneko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.
43. Pomwepo olungamawo adzawalitsa monga dzuwa, mu Ufumu wa Atate wao. Amene ali ndi makutu amve.
44. Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi cuma cobisika m'munda; cimene munthu anacipeza, nacibisa; ndipo m'kucikonda kwace acoka, nagulitsa zonse ali nazo, nagula munda umenewu.
45. Ndiponso Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi munthu wa malonda, wakufuna ngale zabwino:
46. ndipo m'mene anaipeza ngale imodzi ya mtengo wapatari, anapita, nagulitsa zonse anali nazo, naigula imeneyo.
47. Ndiponso, Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi khoka loponyedwa m'nyanja, ndi 1 kusonkhanitsa pamodzi za mitundu yonse;
48. limene podzala, analibvuulira pamtunda; ndipo m'mene anakhala pansi, anazisonkhanitsa zabwino m'zotengera, koma zoipa anazitaya kuthengo.
49. Padzatero pa cimariziro ca nthawi ya pansi pano: angelo adzaturuka, 2 nadzawasankhula oipa pakati pa abwino,
50. nadzawataya m'ng'anjo yamoto; komweko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.
51. Mwamvetsa zonsezi kodi? lwo anati kwa Iye, inde.
52. Ndipo Iye anati kwa iwo, Cifukwa cace, mlembi ali yense, wophunzitsidwa mu Ufumu wa Kumwamba, ali wofanana ndi munthu mwini banja, amene aturutsa m'cuma cace zinthu zakale ndi zatsopano.
53. Ndipo panali, pamene Yesu anatha mafanizo awa, anacokera kumeneko.