Mateyu 13:32-44 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

32. kamene kakhaladi kakang'ono koposa mbeu zonse, koma katakula, kali kakakuru kuposa zitsambazonse, nukhala mtengo, kotero kuti mbalame za mlengalenga zimadza, nizibindikira mu nthambi zace.

33. Fanizo lina ananena kwa iwo; Ufumu wa Kumwamba uli wofanafana ndi cotupitsa mikate, cimene mkazi anacitenga, nacibisa m'miyeso itatu ya ufa, kufikira wonse unatupa.

34. Zonsezi Yesu anaziphiphiritsira m'mafanizo kwa makamu anthu; ndipo kopanda fanizo sanalankhula kanthu kwa iwo;

35. kuti cikacitidwe conenedwa ndi mneneri, kuti,Ndidzatsegula pakamwa panga ndi mafanizo;Ndidzaulula zinthu zobisika ciyambire kukhazikidwa kwace kwa dziko lapansi.

36. Pomwepo Iye anasiya makamuwo, nalowa m'nyumba; ndimo ophunzira ace anadza kwa Iye, nanena, Mutitanthauzire fanizo lija la namsongole wa m'munda.

37. Ndipo Iye anayankha nati, Wofesa mbeu yabwino ndiye Mwana wa munthu;

38. ndipo munda ndiwo dziko lapansi; ndi mbeu yabwino ndiyo ana a Ufumuwo; ndi namsongole ndiye ana a woipayo;

39. ndipo mdani amene anamfesa uwu ndiye mdierekezi: ndi kututa ndico cimariziro ca nthawi ya pansi pano; ndi otutawo ndiwo angelo.

40. Ndipo monga namsongole asonkhanitsidwa pamodzi, natenthedwa pamoto, matero mudzakhala m'cimariziro ca nthawi ya pansi pano.

41. Mwana wa munthu adzatuma angelo ace, ndipo iwo adzasonkhanitsa pamodzi, ndi kucotsa mu Ufumu wace zokhumudwitsa zonse, ndi anthu akucita kusayeruzika,

42. ndipo adzawataya iwo m'ng'anjo yamoto; kumeneko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.

43. Pomwepo olungamawo adzawalitsa monga dzuwa, mu Ufumu wa Atate wao. Amene ali ndi makutu amve.

44. Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi cuma cobisika m'munda; cimene munthu anacipeza, nacibisa; ndipo m'kucikonda kwace acoka, nagulitsa zonse ali nazo, nagula munda umenewu.

Mateyu 13