13. Cifukwa cace ndiphiphiritsira iwo m'mafanizo; cifukwa kuti akuona samaona, ndi akumva samamva, kapena samadziwitsa.
14. Ndipo adzacitidwa kwa iwo mau adanenera Yesaya, amene ati.Pakumva mudzamva, ndipo simudzazindikira konse;Pakupenya mudzapenya, ndipo simudzaona konse;
15. Cifukwa unalemera mtima wa anthuawa,Ndipo m'makutu ao anamva mogontha,Ndipo maso ao anatsinzina;Kuti asaone konse ndi maso,Asamve ndi makutu,Asazindikire ndi mtima wao,Asatembenuke,Ndipo ndisawaciritse iwo.
16. Koma maso anu ali odala, cifukwa apenya; ndi makutu anu cifukwa amva.
17. Pakuti indetu ndinena kwa inu, kuti aneneri ambiri ndi anthu olungama analakalaka kupenya zimene muziona, koma sanaziona; ndi kumva zimene muzimva, koma sanazimva.
18. Ndipo tsono mverani inu fanizolo la wofesa mbeu uja.
19. Munthu ali yense wakumva mau a Ufumu, osawadziwitsai, woipayo angodza, nakwatula cofesedwaco mumtima mwace. Uyo ndiye wofesedwa m'mbali mwa njira.
20. Koma iye amene afesedwa pamiyala, uyu ndiye wakumva mau, ndi kuwalandira pomwepo ndi kusekera;
21. ndipo alibe mizu mwa iye, koma akhala nthawi yaing'ono; ndipo pakudza nsautso kapena zunzo cifukwa ca mau, iye akhumudwa pomwepo.
22. Ndipo iye amene afesedwa kuminga, uyu ndiye wakumva mau; ndipo kulabadira kwa dziko lapansi, ndi cinyengo ca cuma citsamwitsa mau, ndipo akhala wopanda cipatso.
23. Ndipo iye amene afesedwa pa nthaka yabwino, uyu ndiye wakumva mau nawadziwitsa; amene abaladi zipatso, nazifitsa, ena za makumi khumi, ena za makumi asanu ndi limodzi, ena za makumi atatu.