Mateyu 12:28-38 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

28. Koma ngati Ine ndimaturutsa ziwanda ndi mphamvu yace ya Mzimu wa Mulungu, pomwepo Ufumu wa Mulungu unafika pa inu.

29. Kapena akhoza bwanji munthu kulowa m'banja la munthu wolimba, ndi kufunkha akatundu ace, ngati iye sayamba kumanga munthu wolimbayo? ndipo pamenepo adzafunkha za m'banja lace.

30. Iye wosakhala pamodzi ndi Ine akana Ine, ndi iye wosasonkhanitsa pamodzi ndi Ine amwazamwaza.

31. Cifukwa cace ndinena kwa inu, Macimo onse, ndi zonena zonse zamwano, zidzakhululukidwa kwa anthu; koma camwano ca pa Mzimu Woyera sicidzakhululukidwa.

32. Ndipo amene ali yense anganenere Mwana wa munthu zoipa, adzakhululukidwa; koma amene ali yense anganenere Mzimu Woyera zoipa sadzakhululukidwa nthawi yino kapena irinkudzayo.

33. Ukakoma mtengo, cipatso cace comwe cikoma; ukaipa mtengo, cipatso cace comwe ciipa; pakuti ndi cipatso cace mtengo udziwika.

34. Akubadwa inu a njoka, mungathe bwanji kulankhula zabwino, inu akukhala oipa? pakuti m'kamwa mungolankhula mwa kusefuka kwace kwa mtima.

35. Munthu wabwino aturutsa zabwino m'cuma cace cabwino, ndi munthu woipa aturutsa zoipa m'cuma cace coipa.

36. Ndipo ndinena kwa inu, kuti mau onse opanda pace, amene anthu adzalankhula, adzawawerengera mlandu wace tsiku la kuweruza.

37. Pakuti udzayesedwa wolungama ndi mau ako, ndipo ndi mau ako omwe udzatsutsidwa.

38. Pomwepo alembi ndi Afarisi ena anayankha Iye nati, Mphunzitsi, tifuna kuona cizindikiro ca Inu.

Mateyu 12