17. ndi kuti, Tinakulizirani inu zitoliro, ndipo inu simunabvina; tinabuma maliro, ndipo inu simunalira.
18. Pakuti Yohane anadza wosadya, wosamwa, ndipo iwo amati, Ali ndi ciwanda.
19. Mwana wa munthu anadza wakudya, ndi wakumwa, ndipo iwo amati, Onani munthu wakudyaidya ndi wakumwaimwa vinyo, bwenzi la amisonkho ndi ocimwa! Ndipo nzeru iyesedwa yolungama ndi nchito zace.
20. Pomwepo Iye anayamba kutonza midziyo, m'mene zinacitidwa zambiri za nchito zamphamvu zace, cifukwa kuti siinatembenuke.
21. Tsoka kwa iwe, Korazini! tsoka kwa iwe, Betsaida! cifukwa ngati zamphamvu zimene zacitidwa mwa inu zikadacitidwa m'Turo ndi m'Sidoni, akadatembenuka mtima kale kale m'ziguduli ndi m'phulusa.
22. Komanso ndinena kwa inu kuti dzuwa la kuweruza mlandu wao wa Turo ndi Sidoni udzacepa ndi wanu.
23. Ndipo iwe, Kapernao, udzakwezedwa kodi kufikira kuthambo? udzatsika kufikira ku dziko la akufa: cifukwa ngati zamphamvu zimene zacitidwa mwa iwe zikadacitidwa m'Sodomu, uyo ukadakhala kufikira lero.
24. Komanso ndinena kwa im kuti dzuwa la kuweruza, mlandu wace wa Sodomu udzacepa ndi wako.
25. Nyengo imeneyo Yesu anayankha nati, Ndibvomerezana ndi Inu, Atate, Mwini Kumwamba ndi dziko lapansi, kuti munazibisira izo kwa anzeru ndi akudziwitsa, ndipo munaziululira zomwe kwa makanda:
26. etu, Atate, cifukwa cotero cinakhala cokondweretsa pamaso panu.
27. Zinthu zonse zinaperekedwa kwa Ine ndi Atate wanga; ndipo palibe munthu adziwa Mwana, koma Atate yekha; ndi palibe wina adziwa Atate, koma M wana yekha, ndi iye amene Mwana afuna kumuululira.
28. Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu.
29. Senzani gori langa, ndipo phunzirani kwa Ine; cifukwa ndiri wofatsa ndi wodzicepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu.
30. Pakuti 1 gori langa liri lofewa, ndi katundu wanga ali wopepuka.