28. Unacitanso cigololo ndi Aasuri, pakuti unakhala wosakoledwa, inde unacita cigololo nao, koma sunakoledwa.
29. Unacurukitsanso cigololo cako m'dziko la Kanani, mpaka dziko la Akasidi, koma sunakoledwa naconso.
30. Ha! mtima wako ngwofoka, ati Ambuye Yehova, pakucita iwe izi zonse, ndizo nchito za mkazi wacigololo wouma m'maso.
31. Pakumanga nyumba yako yacimphuli pa mphambano ziri zonse, ndi pomanga ciunda cako m'makwalala ali onse, sunakhala ngati mkazi wadama waphindu, popeza unapeputsa mphotho.
32. Ndiwe mkazi wokwatibwa wocita cigololo, wolandira alendo m'malo mwa mwamuna wace.
33. Anthu amaninkha akazi onse acigololo mphatso, koma iwe umaninkha mabwenzi ako onse mphatso zako ndi kuwalipira, kuti akudzere kucokera ku mbali zonse, kuti acite nawe cigololo.
34. M'mwemo usiyana konse ndi akazi ena m'cigololo cako; pakuti palibe wokutsata kucita nawe cigololo; popezanso uwalipira, koma sakupatsa iwe mphotho; potero usiyana nao konse ena.
35. Cifukwa cace, wacigololo iwe, tamvera mau a Yehova:
36. Atero Ambuye Yehova, Popeza ndalama zako zamwazika, nubvundukuka umarisece wako mwa cigololo cako ndi mabwenzi ako, ndi cifukwa ca mafano onse a zonyansa zako, ndi mwazi wa ana ako umene unawa patsa;
37. cifukwa cace taona, ndidzasonkhanitsa mabwenzi ako onse amene wakondwera nao, ndi onse unawakonda, pamodzi ndi onse unawada; inde ndidzawasonkhanitsira iwe pozungulira ponse, ndi kuwabvundukulira umarisece wako, kuti aone umarisece wako wonse.
38. Ndipo ndidzaweruza mlandu wako, monga aweruza akazi acigololo ndi okhetsa mwazi; ndipo ndidzakutengera mwazi wa ukali ndi wa nsanje.
39. Ndidzakuperekanso m'dzanja lao, ndipo adzagwetsa nyumba yako yacimphuli, ndi kugumula ziunda zako, nadzakubvula zobvala zako, ndi kulanda zokometsera zako zokongola, nadzakusiya wamarisece ndi wausiwa.
40. Ndipo adzamemezera iwe msonkhano, nadzakuponya miyala, ndi kukupyoza ndi malupanga ao.
41. Ndipo adzatentha nyumba zako ndi moto, nadzakuweruza pamaso pa akazi ambiri; ndipo ndidzakuleketsa kucita cigololo, ndipo sudzalipiranso mphotho yacigololo.
42. M'mwemo ukali wanga udzakhuta nawe, ndi nsanje yanga idzakucokera, ndipo ndidzakhala cete wosakwiyanso.
43. Popeza sunakumbukila masiku a ubwana wako, koma wandibvuta nazo zonsezi, cifukwa cace taona, Inenso ndidzakubwezera njira yako pamutu pako, ati Ambuye Yehova; ndipo sudzacita coipa ici coonjezerapo pa zonyansa zako zonse.