12. Ndipo anakwaniritsa mau ace adanenawo, kutitsutsa ife ndi oweruza athu otiweruza, ndi kutitengera coipa cacikuru; pakuti pansi pa thambo lonse sipanacitika monga umo panacitikira Yerusalemu.
13. Monga mulembedwa m'cilamulo ca Mose coipa ici conse catidzera; koma sitinapepeza Yehova Mulungu wathu, ndi kubwera kuleka mphulupulu zathu, ndi kucita mwanzeru m'coonadi canu.
14. Cifukwa cace Yehova wakhala maso pa coipaco, ndi kutifikitsira ico; pakuti Yehova Mulungu wathu ali wolungama mu nchito zace zonse azicita; ndipo sitinamvera mau ace.