Caka cacitatu ca Koresi mfumu ya Perisiya, cinabvumbulutsidwa cinthu kwa Danieli, amene anamucha Belitsazara; ndipo cinthuco ncoona, ndico nkhondo yaikuru; ndipo anazindikira cinthuco, nadziwa masomphenyawo.