Danieli 11:12-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndipo ataucotsa unyinjiwo udzakwezeka mtima wace; ndipo adzagwetsa zikwi makumi makumi, koma sadzalakika.

13. Ndi mfumu ya kumpoto idzabwera, nidzaimika unyinji wa kuposa oyamba aja; nidzafika pa cimariziro ca nthawi, ca zaka, ndi khamu lalikuru la nkhondo ndi cuma cambiri.

14. Ndipo nthawi zija ambiri adzaukira mfumu ya kumwela, ndi aciwawa mwa anthu a mtundu wako adzadzikuza kukhazikitsa masomphenyawo, koma adzagwa iwo.

15. Ndi mfumu ya kumpoto idzadza, nidzaunda mtumbira, nidzalanda midzi yamalinga; ndi ankhondo a kumwela sadzalimbika, ngakhale anthu ace osankhika; inde sipadzakhala mphamvu yakulimbika.

16. Koma iye amene amdzera kulimbana naye adzacita cifuniro cace ca iye mwini; palibe wakulimbika pamaso pace; ndipo adzaima m'dziko lokometsetsalo, ndi m'dzanja mwace mudzakhala cionongeko.

17. Ndipo adzalimbitsa nkhope yace, kudza ndi mphamvu ya ufumu wace wonse, ndi oongoka mtima pamodzi naye; ndipo adzacita cifuniro cace, nadzampatsa mwana wamkazi wa akazi kumuipitsa; koma mkaziyo sadzalimbika, kapena kubvomerezana naye.

18. Pambuyo pace adzatembenuzira nkhope yace kuzisumbu, nadzalanda zambiri; koma kalonga wina adzaleketsa kunyoza kwace adanyoza nako; inde adzambwezera yekha kunyoza kwace.

19. Pamenepo adzatembenuzira nkhope yace ku malinga a dziko lace lace; koma adzakhumudwa, nadzagwa osapezedwanso.

Danieli 11