2 Mbiri 29:25-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

25. Ndipo anaika Alevi m'nyumba ya Yehova ndi nsanje, ndi zisakasa, ndi azeze, monga umo adauzira Davide, ndi Gadi mlauli wa mfumu, ndi Natani mneneriyo; pakuti lamulo ili lidafuma kwa Yehova mwa aneneri ace.

26. Alevi tsono anaimirira ndi zoyimbira za Davide, ndi ansembe anakhala ndi malipenga.

27. Nanena Hezekiya kuti apereke nsembe yopsereza pa guwa la nsembe. Ndipo pakuyamba nsembe yopsereza, inayambanso nyimbo ya Yehova ndi malipenga, pamodzi ndi zoyimbira za Davideyo mfumu ya Israyeli.

28. Ndi msonkhano wonse unalambira, ndi oyimbira anayimba, ndi amalipenga anaomba; zonsezi mpaka adatsiriza nsembe yopsereza.

29. Ndipo atatsiriza kuperekaku, mfumu ndi onse opezeka pamodzi naye anawerama, nalambira.

30. Hezekiya mfumu ndi akalonga anauzanso Alevi ayimbire Yehova zomlemekeza ndi mau a Davide ndi a Asafu mlauli. Ndipo anayimbira zomlemekeza mokondwera, nawerama mitu yao, nalambira.

31. Pamenepo Hezekiya anayankha, nati, Tsopano mwadzipatulira kwa Yehova, senderani, bwerani nazo nsembe zophera ndi nsembe zoyamika ku nyumba ya Yehova. Ndi msonkhano unabwera nazo nsembe zophera ndi nsembe zoyamika, ndi onse a mtima wofuna mwini anabwera nazo nsembe zopsereza.

2 Mbiri 29