5. Ndipo kunali, pakumva ici Basa, analeka kumangitsa Rama, naleketsa nchito yace.
6. Pamenepo Asa mfumu anatenga Ayuda onse, ndipo anatuta miyala ya ku Rama, ndi mitengo yace, imene Basa adamanga nayo, namangira Geba ndi Mizipa.
7. Nthawi yomweyi Hanani mlauli anadza kwa Asa mfumu ya Yuda, nanena naye, Popeza mwatama mfumu ya Aramu, osatama Yehova Mulungu wanu, cifukwa cace khamu la nkhondo la mfumu ya Aramu lapulumuka m'dzanja lanu.
8. Nanga Akusi ndi Alubi, sanakhala khamu lalikurukuru, ndi magareta ndi apakavalo ambirimbiri, koma muja munatama Yehova anawapereka m'dzanja mwanu?
9. Pakuti maso a Yehova ayang'ana uko ndi uko m'dziko lonse lapansi, kudzionetsera wamphamvu kwa iwo amene mtima wao uli wangwiro ndi Iye. Mwacita copusa m'menemo; pakuti kuyambira tsopano mudzaona nkhondo.
10. Koma Asa anakwiya naye mlauliyo, namuika m'kaidi; pakuti adapsa mtima naye cifukwa ca ici. Nthawi yomweyi Asa anasautsa anthu ena.
11. Ndipo taonani, zocita Asa, zoyamba ndi zotsiriza, zalembedwa m'buku la mafumu a Yuda ndi Israyeli.