1. Ndipo kunali tsiku lina kuti Jonatani mwana wa Sauli ananena ndi mnyamata wonyamula zida zace, Tiye tipite kunka ku kaboma ka Afilisti, tsidya lija. Koma sanauza atate wace.
2. Ndipo Sauli analikukhala m'matsekerezo a Gibeya patsinde pa mtengo wankhangaza uli ku Migroni; ndipo panali naye anthu monga mazana asanu ndi limodzi;
3. ndi Ahiya mwana wa Ahitubi mbale wace wa Ikabodi, mwana wa Pinehasi, mwana wa Eli, wansembe wa Yehova wa ku Silo, wobvala efodi. Ndipo anthuwo sanadziwa kuti Jonatani wacoka.