1 Mbiri 22:7-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Ndipo Davide anati kwa Solomo mwana wace, Kunena za ine, kumtima kwanga kudati, ndilimangire dzina la Yehova Mulungu wanga nyumba.

8. Koma mau a Yehova anandidzera, kuti, Wakhetsa mwazi wocuruka, popeza wacita nkhondo zazikuru; sudzamangira dzina langa nyumba, popeza wakhetsa pansi mwazi wambiri pamaso panga;

9. taona, udzabala mwana, ndiye adzakhala munthu wa phe; ndipo nelidzampumulitsira adani ace onse pozungulirapo, pakuti dzina lace lidzakhala Solomo; ndipo ndidzapatsa Israyeli mtendere ndi bata masiku ace;

10. iyeyu adzamangira dzina langa nyumba; iye adzakhala mwana wanga, ndi Ine ndidzakhala Atate wace; ndipo ndidzakhazikitsa mpando wacifumu wa ufumu wace pa Israyeli kosalekeza.

11. Tsono, mwana wanga, Yehova akhale nawe; nulemerere, numange nyumba ya Yehova Mulungu wako monga ananena za iwe.

12. Cokhaci, Yehova akupatse nzeru ndi luntha, nakulangize za Israyeli, kuti usunge cilamulo ca Yehova Mulungu wako,

13. Momwemo udzalemerera, ukasamalira kucita malemba ndi maweruzo amene Yehova analangiza Mose za Israyeli; limbikatu, nulimbike mtima, usaope, usade mtima.

14. Taona tsono, m'kuzunzika kwanga ndinakonzeratu nyumba ya Yehova matalente zikwi zana limodzi a golidi, ndi matalente zikwi zikwi a siliva, ndi mkuwa, ndi citsulo, osayesa kulemera kwace, pakuti zidacurukaeli; mitengo yomwe ndi miyala ndakonzeratu; nuonjezereko.

15. Uli naonso anchito ocuruka ofukula miyala, ndi amisiri a miyala ndi a mitengo, ndi amuna onse aluso akucita nchito ziri zonse;

16. golidi, ndi siliva, ndi mkuwa, ndi citsulo, nzosawerengeka; nyamuka, nucite, Yehova akhale nawe.

17. Davide analangizanso akalonga a Israyeli athanelize Solomo mwana wace, ndi kuti,

1 Mbiri 22