6. Nati Davide, Ali yense woyamba kukantha Ayebusi, yemweyo adzakhala mkulu ndi mtsogoleri. Nayamba kukwerako Yoabu mwana wa Zeruya, nakhala mkuru iyeyu.
7. Ndipo Davide anakhala m'lingamo; cifukwa cace analicha mudzi wa Davide.
8. Ndipo anamanga mudzi pozungulira pace, kuyambira ku Milo ndi pozungulira pace; ndi Yoabu anakonzanso potsala pa mudzi.
9. Ndipo Davide anakula-kulabe, pakuti Yehova wa makamu anali naye.
10. Akuru a amphamvu aja Davide anali nao akulimbika pamodzi naye m'ufumu wace, pamodzi ndi Aisrayeli onse, kumlonga ufumu, monga mwa mau a Yehova akunena za Israyeli, ndi awa.
11. Kuwerenga kwa amphamvu aja Davide anali nao ndi uku: Yasobeamu mwana wa Mhakimoni, mkuru wa makumi atatu aja, anasamulira mazana atatu mkondo wace, nawapha nthawi imodzi.
12. Ndi pambuyo pace Eleazara mwana wa Dodo M-ahohi, ndiye mmodzi wa atatu aja amphamvu.
13. Anali pamodzi ndi Da vide ku Pasidamimu muja; Afilisti anasonkhanako kunkhondo kumene kunali munda wodzala ndi barele; ndipo anthu anathawa pamaso pa Afilisti.