1 Mbiri 11:11-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Kuwerenga kwa amphamvu aja Davide anali nao ndi uku: Yasobeamu mwana wa Mhakimoni, mkuru wa makumi atatu aja, anasamulira mazana atatu mkondo wace, nawapha nthawi imodzi.

12. Ndi pambuyo pace Eleazara mwana wa Dodo M-ahohi, ndiye mmodzi wa atatu aja amphamvu.

13. Anali pamodzi ndi Da vide ku Pasidamimu muja; Afilisti anasonkhanako kunkhondo kumene kunali munda wodzala ndi barele; ndipo anthu anathawa pamaso pa Afilisti.

14. Koma anadziimika pakati pa munda, naulanditsa, nakantha Afilisti; m'mwemo anawapulumutsa Yehova ndi cipulumutso cacikuru.

15. Ndipo atatu a akuru makumi atatu anatsikira kuthanthwe kwa Davide, ku phanga la Adulamu; ndi nkhondo ya Afilisti idamanga misasa m'cigwa ca Refaimu.

16. Pamenepo Davide anali m'linga, ndi boma la askari linali ku Betelehemu.

17. Ndipo Davide analakalaka, nati, Ha! mwenzi wina atandimwetsa madzi a m'citsime ca ku Betelehemu ciri kucipata,

18. Napyola atatuwo misasa ya Afilish natunga madzi ku citsime ca ku Betelehemu ciri kucipata, nabwera nao kwa Davide; koma Davide anakana kumwako, koma anawathirira kwa Yehova;

19. nati, Pali Mulungu wanga, kukhale kutali kwa ine kucita ici. Ngati ndidzamwa mwazi wa anthu awa? Akadataya moyo wao, inde akadataya moyo wao, pakukatenga madziwa. M'mwemo sanafuna kuwamwa. Izi anazicita atatu amphamvuwa.

20. Ndipo Abisai mbale wa Yoabu, ndiye wamkuru wa atatuwa; pakuti anasamulira mazana atatu mkondo wace, nawapha, namveka dzina pakati pa atatuwa.

21. Mwa atatuwa iye anali waulemu woposa awiriwa, nasanduka mkuru wao; koma sanafikana nao atatu oyamba aja.

22. Benaya mwana wa Yehoyada, mwana wa ngwazi ya ku Kabzeeli, wocita zazikuru, anapha ana awiri a Ariyeli wa ku Moabu; anatsikanso, napha mkango m'kati mwa dzenje nyengo ya cipale cofewa.

1 Mbiri 11