Benaya mwana wa Yehoyada, mwana wa ngwazi ya ku Kabzeeli, wocita zazikuru, anapha ana awiri a Ariyeli wa ku Moabu; anatsikanso, napha mkango m'kati mwa dzenje nyengo ya cipale cofewa.