1 Mbiri 11:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pamenepo Aisrayeli onse anasonkhana kwa Davide ku Hebroni, ndi kuti, Taonani, ife ndife pfupa lanu, ndi mnofu wanu.

2. Ngakhale kale lomwe, pokhala mfumu Sauliyo, woturuka ndi kulowa nao Aisrayeli ndinu; ndipo Yehova Mulungu wanu anati kwa inu, Uzidyetsa anthu anga Aisrayeli, nukhale mtsogoleri wa anthu anga Israyeli.

3. Akuru onse omwe a Israyeli anadza kwa mfumu ku Hebroni; ndipo Davide anapangana nao pangano ku Hebroni pamaso pa Yehova; ndipo anamdzoza Davide akhale mfumu ya Israyeli monga mwa mau a Yehova, ndi lizanja la Samueli.

4. Namuka Davide ndi Aisrayeli onse naye ku Yerusalemu, ndiwo Yebusi; ndipo Ayebusi nzika za m'dziko zinali komweko.

5. Ndipo nzika za m'Yebusi zinati kwa Davide, Sungalowe muno. Koma Davide analanda linga la Ziyoni, ndiwo mudzi wa Davide.

6. Nati Davide, Ali yense woyamba kukantha Ayebusi, yemweyo adzakhala mkulu ndi mtsogoleri. Nayamba kukwerako Yoabu mwana wa Zeruya, nakhala mkuru iyeyu.

7. Ndipo Davide anakhala m'lingamo; cifukwa cace analicha mudzi wa Davide.

8. Ndipo anamanga mudzi pozungulira pace, kuyambira ku Milo ndi pozungulira pace; ndi Yoabu anakonzanso potsala pa mudzi.

9. Ndipo Davide anakula-kulabe, pakuti Yehova wa makamu anali naye.

1 Mbiri 11