8. Ndipo akulu onse ndi anthu onse anati kwa iye, Musamvere, musabvomereze.
9. Ndipo anati kwa mithenga ya Benihadadi, Kauzeni mbuye wanga mfumu, Zonse munayamba kundituma mtumiki wanu kuzifunsa ndidzacita, koma ici sindingacicite. Nicoka mithengayo, nimbwezera mau.
10. Ndipo Benihadadi anatuma kwa iye, nati, Milungu indilange, nionjezepo, ngati pfumbi la Samaria lidzafikira kudzaza manja a anthu onse akutsata mapazi anga.
11. Ndipo mfumu ya Israyeli anayankha, nati, Kamuuzeni, Wakumanga zida asadzikuze ngati wakubvulayo.
12. Ndipo kunacitika, atamva Benihadadi mau awa, analikumwa nao mafumu m'misasa, ananena ndi anyamata ace, Nikani. Nandandalika pamudzipo.
13. Ndipo taonani, mneneri anadza kwa Ahabu mfumu ya Israyeli, nati, Atero Yehova, Kodi waona unyinji uwu waukuru wonse? Taonani, ndidzaupereka m'dzanja mwako lero, kuti udziwe kuti ndine Yehova.