7. Haya Ziyoni, thawa iwe wakukhala ndi mwana wamkazi wa Babulo.
8. Pakuti atero Yehova wa makamu: Utatha ulemererowo ananditumiza kwa amitundu amene anakufunkhani; pakuti iye wokhudza inu, akhudza mwana wa m'diso lace.
9. Pakuti, taonani, ndidzawayambasira dzanja langa, ndipo adzakhala zofunkha za iwo amene anawatumikira; ndipo mudzadziwa kuti Yehova wa makamu anandituma.
10. Yimba, nukondwere, mwana wamkazi wa Ziyoni; pakuti taonani, ndirinkudza, ndipo ndidzakhala pakati pako, ati Yehova.
11. Ndipo amitundu ambiri adzaphatikidwa kwa Yehova tsiku ilo, nadzakhala anthu anga; ndipo ndidzakhala pakati pako, ndipo udzadziwa kuti Yehova wa makamu anandituma kwa iwe.
12. Ndipo Yehova adzalandira colowa cace Yuda, ngati gawo lace m'dziko lopatulikalo, nadzasankhanso Yerusalemu.