Zekariya 13:2-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Ndipo kudzacitika tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, ndidzaononga maina a mafano m'dziko; ndipo sadzakumbukikanso; ndipo ndidzacotsa m'dziko aneneri ndi mzimu wacidetso.

3. Ndipo kudzacitika, akaneneranso wina, atate wace ndi mai wace ombala adzanena naye, Sudzakhala ndi moyo, pakuti unena bodza m'dzina la Yehova; ndipo atate wace ndi mai wace ombala adzamgwaza ponenera iye.

4. Ndipo kudzacitika tsiku lomwelo kuti aneneri adzacita manyazi yense ndi masomphenya ace, ponenera iye; ndipo sadzabvala copfunda caubweya kunyenga naco;

Zekariya 13