4. Koma mkaziyo anatenga amuna awiriwo, nawabisa; natero, Inde, amunawo anandifikira; koma sindinadziwa uko afuma;
5. ndipo m'mene akadati atseke pacipata, kutada, anaturuka amunawo; uko anamuka amunawo osakudziwa ine; muwalondole msanga, pakuti mudzawapeza.
6. Koma adawakweretsa patsindwi, nawabisa ndi mitengo yanthamza yoyanika patsindwi.
7. Ndipo amunawo anawalondola pa njira ya ku Yordano yomka kudooko; ndipo ataturuka akuwalondola, anatseka pacipata.
8. Koma asanagone iwo, anawakwerera patsindwi iye,
9. nati kwa amunawo, Ndidziwa kuti Yehova wakupatsani dzikoli, ndi kuti kuopsa kwanu kwatigwera, ndi kuti okhala m'dziko onse asungunuka pamaso panu.
10. Popeza tidamva kuti Yehova anaphwetsa madzi a m'Nyanja Yofiira pamaso panu, muja mudaruruka m'Aigupto; ndi cija munacitira mafumu awiri a Aamori okhala tsidya la Yordano, ndiwo Sihoni ndi Ogi, amene mudawaononga konse.