23. Koma Yesu anayankha iwo, nati, Yafika nthawi, kuti Mwana wa munthu alemekezedwe.
24. Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Ngati mbeu ya tirigu siigwa m'nthaka, nifa, ikhala pa yokha iyo; koma ngati ifa, ibala cipatso cambiri.
25. Iye wokonda moyo wace adzautaya; ndipo wodana ndi moyo wace m'dziko lino lapansi adzausungira ku moyo wosatha.
26. Ngati wina anditumikira Ine, anditsate; ndipo kumene kuli Ine, komwekonso kudzakhala mtumiki wanga, Ngati wina anditumikira Ine, Atate adzamcitira ulemu iyeyu,
27. Moyo wanga wabvutika tsopano; ndipo ndidzanena ciani? Atate, ndipulumutseni Ine ku nthawi iyi. Koma cifukwa ca ici ndinadzera nthawi iyi.
28. Atate, lemekezani dzina lanu. Pomwepo adadza mau ocokera Kumwamba, ndalilemekeza, ndipo ndidzalilemekezanso.