Yesaya 45:18-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Pakuti atero Yehova amene analenga kumwamba, Iye ndiye Mulungu amene anaumba dziko lapansi, nalipanga; Iye analikhazikitsa, sanalilenga mwacabe; Iye analiumba akhalemo anthu; Ine ndine Yehova; ndipo palibenso wina.

19. Ine sindinanena m'tseri m'malo a dziko la mdima; Ine sindinati kwa mbeu ya Yakobo, Mundifune Ine mwacabe; Ine Yehova ndinena cilungamo, ndinena zimene ziri zoona.

20. Sonkhanani nokha, mudze; yandikirani cifupi pamodzi, inu amene mwapulumuka amitundu; iwo alibe nzeru, amene anyamula mtengo wa fano lao losema, ndi kupemphera mlungu wosakhoza kupulumutsa.

21. Nenani inu, turutsani mlandu wanu; inde, acite uphungu pamodzi; ndani waonetsa ici ciyambire nthawi yakale? ndani wanena ici kale? kodi si ndine Yehova? ndipo palibenso Mulungu wina popanda Ine; Mulungu wolungama, ndi Mpulumutsi; palibenso wina popanda Ine.

22. Yang'anani kwa Ine, mupulumutsidwe, inu malekezero onse a dziko; pakuti Ine ndine Mulungu, palibe wina.

Yesaya 45