Yesaya 38:6-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo ndidzakupulumutsa iwe ndi mudzi uno m'manja mwa mfumu ya Asuri, ndipo ndidzacinjiriza mudzi uno.

7. Ndipo ici cidzakhala cizindikilo kwa iwe cocokera kwa Yehova, kuti Yehova adzacita ici wanenaci;

8. taona, ndidzabweza mthunzi wa pamakwerero, umene watsika pa makwerero a Ahazi ndi dzuwa, ubwerere makwerero khumi. Ndipo dzuwa linabwerera makwerero khumi pamakwerero, pamene udatsika mthunziwo.

9. Malemba a Hezekiya mfumu ya Ayuda muja anadwala, atacira nthenda yace.

10. Ine ndinati, Pakati pa masiku anga ndidzalowa m'zipata za kunsi kwa manda; Ndazimidwa zaka zanga zotsala.

11. Ndinati, Sindidzaona Yehova m'dziko la amoyo; sindidzaonanso munthu pamodzi ndi okhala kunja kuno;

12. Pokhala panga pacotsedwa, pandisunthikira monga hema wambusa;Ndapindapinda moyo wanga ngati muomba;Iye adzandidula ine poomberapo;Kuyambira usana kufikira usiku mudzanditsiriza ine.

Yesaya 38