5. Pakuti mukakonzatu njira zanu ndi macitidwe anu; ndi kuweruzatu milandu ya munthu ndi mnansi wace;
6. ndi kuleka kutsendereza mlendo, ndi wamasiye, ndi mkazi wamasiye, osakhetsa mwazi wosacimwa m'malo muno, osatsata milungu yina ndi kudziipitsa nayo;
7. ndipo ndidzakukhazikani inu m'malo muno, m'dziko limene ndinapatsa makolo anu, kuyambira kale lomwe kufikira muyaya,
8. Taonani, mukhulupirira mau onama, osapindulitsa.
9. Kodi mudzapha, ndi kuba, ndi kucita cigololo, ndi kulumbira zonama, ndi kupereka nsembe kwa Baala, ndi kutsata milungu yina imene simunaidziwa,
10. ndi kudza ndi kuima pamaso panga m'nyumba yino, imene ichedwa dzina langa, ndi kuti, Talanditsidwa; kuti mucite zonyansa izi?
11. Kodi nyumba yino, imene ichedwa dzina langa, ikhala phanga la okwatula pamaso panu? Taona, Ine ndaciona, ati Yehova.