50. Inu amene mwapulumuka kulupanga, pitani inu, musaime ciimire; mukumbukire Yehova kutari, Yerusalemu alowe m'mtima mwanu.
51. Tiri ndi manyazi, cifukwa tamva mnyozo; manyazi aphimba nkhope zathu; pakuti alendo alowa m'malo opatulika a nyumba ya Yehova.
52. Cifukwa cace, taona, masiku alinkudza, ati Yehova, amene ndidzaweruza mafano ace; ndipo pa dziko lace lonse olasidwa adzabuula.
53. Ngakhale Babulo adzakwera kumwamba, ngakhale adzalimbitsa msanje wa mphamvu yace, koma kucokera kwa Ine akufunkha adzafika kwa iye, ati Yehova.
54. Mau akupfuula ocokera ku Babulo, ndi a cionongeko cacikuru ku dziko la Akasidi!
55. pakuti Yehova afunkha Babulo, aononga m'menemo mau akuru; ndipo mafunde ace adzakokoma ngati madzi ambiri, mau ao aphokosera;
56. pakuti wakufunkha wafika kwa iye, kwa Babulo, ndi anthu ace olimba agwidwa, mauta ao atyokatyoka, pakuti Yehova ndiye Mulungu wakubwezera, adzabwezera ndithu.