43. Midzi yace yakhala bwinja, dziko louma, cipululu mosakhalamo anthu, mosapita mwana wa munthu ali yense.
44. Ndipo Ine ndiweruza Beli m'Babulo, ndipo ndidzaturutsa m'kamwa mwace comwe wacimeza; ndipo amitundu sadzasonkhaniranso konse kwa iye; inde, khoma la Babulo lidzagwa.
45. Anthu anga, turukani pakati pace, mudzipulumutse munthu yense ku mkwiyo waukali wa Yehova.
46. Mtima wanu usalefuke, musaope cifukwa ca mbiri imene idzamveka m'dzikomu; pakuti mbiri idzafika caka cina, pambuyo pace caka cina mbiri yina, ndi ciwawa m'dziko, wolamulira kumenyana ndi wolamulira.
47. Cifukwa cace, taonani, masiku alinkudza, amene ndidzaweruza mafano osemasema a Babulo, ndipo dziko lace lonse lidzakhala ndi manyazi; ndipo ophedwa ace onse adzagwa pakati pace.
48. Pamenepo kumwamba ndi dziko lapansi, ndi zonse ziri m'menemo, zidzayimba mokondwerera Babulo; pakuti akufunkha adzafika kwa iye kucokera kumpoto, ati Yehova.
49. Monga Babulo wagwetsa ophedwa a Israyeli, momwemo pa Babulo padzagwa ophedwa a dziko lonse.
50. Inu amene mwapulumuka kulupanga, pitani inu, musaime ciimire; mukumbukire Yehova kutari, Yerusalemu alowe m'mtima mwanu.