Yeremiya 16:5-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Pakuti Yehova atero, Usalowe m'nyumba ya maliro, usanke kukacita maliro ao, kapena kuwalirira; pakuti ndacotsa mtendere wanga pa anthu awa, cifundo ndi nsoni zokoma, ati Yehova.

6. Akuru ndi ang'onong'ono adzafa m'dziko muno; sadzaikidwa, anthu sadzacita maliro ao, sadzadziceka, sadzadziyeseza adazi, cifukwa ca iwo;

7. anthu sadzawagawira mkate pamaliro, kuti atonthoze mitima yao cifukwa ca akufa, anthu sadzapatsa iwo cikho ca kutonthoza kuti acimwe cifukwa ca atate ao kapena mai wao.

8. Usalowe m'nyumba ya madyerero kukhala nao, ndi kudya ndi kumwa.

9. Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli; Taonani, ndidzaletsa pano, pamaso panu masiku anu, mau akukondwerera ndi mau akusangalala, mau a mkwati ndi mau a mkwatibwi.

Yeremiya 16