Oweruza 8:4-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndipo Gideoni anafika ku Yordano, naoloka, iye ndi amuna mazana atatu anali naye, ali otopa koma ali cilondolere.

5. Ndipo ananena kwa amuna a ku Sukoti, Mupatsetu anthu awa akunditsata mitanda yamkate; pakuti atopa, ndipo ndirikulondola Zeba ndi Tsalimuna mafumu a Midyani.

6. Koma akalonga a ku Sukoti anati, Kodi manja a Zeba ndi Tsalimuna ali m'dzanja lako tsopano apa, kuti ife tiwaninkhe ankhondo ako mkate?

7. Ndipo Gideoni anati, Cifukwa cace, Yehova akapereka Zeba ndi Tsalimuna m'dzanja langa, ndidzapuntha nyama yanu ndi minga ya m'cipululu ndi mitungwi.

8. Ndipo anacokapo kukwera ku Penueli, nanena nao momwemo; ndipo amuna a ku Penueli anamyankha monga adamyankha amuna a ku Sukoti.

Oweruza 8