Oweruza 7:3-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Ndipo tsopano, kalalike m'makutu a anthu, ndi kuti, Ali yense wocita mantha, nanjenjemera, abwerere nacoke pa phiri la Gileadi. Ndipo anabwererako anthu zikwi makumi awiri mphambu ziwiri, natsalako zikwi khumi.

4. Ndipo Yehova ananena ndi Gideoni, Anthu akali ocuruka; tsikira nao kumadzi, ndipo ndidzakuyesera iwo komweko; ndipo kudzali kuti iye amene ndimnena kwa iwe, Uyo azimuka nawe, yemweyo azimuka nawe; koma ali yense ndimnena kwa iwe, Uyo asamuke nawe, yemweyo asamuke.

5. Ndipo anatsikira nao anthu kumadzi; ndipo Yehova anati kwa Gideoni, Ali yense akapiza madzi pa lilime lace, monga akhatira garu, ameneyo amuike pa yekha; momwemo ali yense agwada pakumwa.

6. Ndi kuwerenga kwa iwo akukhatira, ndi kuika dzanja lao kukamwa kwao, ndiko mazana atatu; koma ena onse anagwada pakumwa madzi.

7. Ndipo Yehova anati kwa Gideoni, Ndi anthu mazana atatu akukhatira ndidzakupulumutsani, ndi kupereka Amidyani m'dzanja lako; koma amuke anthu awa onse, yense kumalo kwace.

8. Pamenepo anthu anatenga kamba m'dzanja lao, ndi malipenga ao; ndipo anauza amuna onse a Israyeli amuke, yense kuhema kwace; koma anaimika amuna mazana atatuwo; ndipo misasa ya Midyani inali kunsi kwace m'cigwa.

9. Ndipo kunali usiku womwewo, kuti Yehova ananena naye, Tauka, tatsikira kumisasa; pakuti ndaipereka m'dzanja lako.

10. Koma ngati uopa kutsika, utsike naye Pura mnyamata wako kumisasa;

Oweruza 7