Ndipo anatsikira nao anthu kumadzi; ndipo Yehova anati kwa Gideoni, Ali yense akapiza madzi pa lilime lace, monga akhatira garu, ameneyo amuike pa yekha; momwemo ali yense agwada pakumwa.