Ndipo tsopano, kalalike m'makutu a anthu, ndi kuti, Ali yense wocita mantha, nanjenjemera, abwerere nacoke pa phiri la Gileadi. Ndipo anabwererako anthu zikwi makumi awiri mphambu ziwiri, natsalako zikwi khumi.