Oweruza 6:33-40 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

33. Pamenepo Amidyani onse ndi Aamaleki ndi ana a kum'mawa anasonkhana pamodzi naoloka, namanga misasa m'cigwa ca Yezreeli.

34. Koma mzimu wa Yehova unabvana Gideoni; naomba lipenga iye, ndi a banja la Abieziri analalikidwa kumtsata iye.

35. Ndipo anatuma mithenga kwa Manase konse; ndi iwonso analalikidwa kumtsata iye; natuma mithenga kwa Aseri, ndi kwa Zebuloni, ndi kwa Nafitali; iwo nadzakomana nao.

36. Ndipo Gideoni anati kwa Mulungu, Mukadzapulumutsa Israyeli ndi dzanjalanga monga mwanena,

37. taonani, ndidzaika cikopa ca ubweya popunthira tirigu; pakakhala mame pacikopa pokha, ndi panthaka ponse pouma, pamenepo ndidzadziwa kuti mudzapulumutsa Israyeli ndi dzanja langa monga mwanena.

38. Ndipo kunatero; pakuti anauka mamawa, nafinya cikopaco, nakamula mame a pacikopa, madzi ace odzala mbale.

39. Ndipo Gideoni ananena ndi Mulungu, Mkwiyo wanu usandiyakire, ndinene kamodzi kokha: ndikuyeseni kamodzi kokha ndi cikopa; paume pacikopa pokha, ndi panthaka ponse pakhale mame.

40. Ndipo Mulungu anatero usiku uja; pakuti panauma pacikopa pokha, ndi panthaka ponse panali mame.

Oweruza 6