Oweruza 20:40-48 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

40. Koma pamene mtambo unayamba kukwera m'mudzi ngati utsi uti tolo, Abenjamini anaceuka, ndipo taonani, pamodzi ponse panafuka utsi kumwamba.

41. Natembenuka amuna a Israyeli; nadabwa amuna a Benjamini; popeza anaona kuti cidawagwera coipa.

42. Nabwerera iwo pamaso pa amuna a Israyeli kumka njira ya cipululu; koma nkhondo inawaloodetsa; ndi aja oturuka m'mudzi anawaononga pakati pao.

43. Anawazinga Abenjamini, anawapitikitsa, nawapondereza pampumulo mpaka pandunji pa Gibeya, koturukira dzuwa.

44. Ndipo adagwa a Benjamini amuna zikwi khumi ndi zisanu ndi zitatu; iwo onse ndiwo ngwazi.

45. Natembenuka iwo, nathawira kucipululu ku thanthwe la Rimoni; koma anawakunkha m'makwalala amuna zikwi zisanu; nawalondetsa ku Gidomu, nakantha a iwowa amuna zikwi ziwiri.

46. Potero onse amene adagwa a Benjamini tsiku lija, ndiwo amuna zikwi makumi awiri mphambu zisanu, akusolola lupanga; iwo onse ndiwo ngwazi.

47. Koma amuna mazana asanu ndi limodzi anabwerera nathawira kucipululu, ku thanthwe la Rimoni, nakhala m'thanthwe la Rimoni miyezi inai.

48. Ndipo amuna a Israyeli anabwereranso kwa ana a Benjamini, nawakantha ndi lupanga lakuthwa a m'mudzi wonse, ndi zoweta, ndi zonse adazipeza; anatenthanso midzi yonse anaipeza.

Oweruza 20