34. Ndipo anadza pandunji pa Gibeya amuna osankhika m'Israyeli monse zikwi khumi, nikula nkhondo; koma sanadziwa kuti coipa ciri pafupi kuwakhudza.
35. Ndipo Yehova anakantha Benjamini pamaso pa Israyeli; ndi ana a Israyeli anawaononga a Benjamini tsiku lija amuna zikwi makumi awiri ndi zisanu, kudza zana limodzi; awa onse ndiwo akusolola lupanga.
36. Ndipo ana a Benjamini anaona kuti takanthidwa; popeza amuna a Israyeli anawapatsa Abenjamini malo, pakuti anatama olalira amene anawaikiratu pa Gibeya.
37. Nafulumira olalirawo nathamangira Gibeya, nabalalika olalirawo, nakantha mudzi wonse ndi lupanga lakuthwa.
38. Koma kunali cizindikilo coikika pakati pa amuna a Israyeli ndi olalirawo, ndico cakuti afukitse mtambo wa utsi kumudzi.
39. Ndi nkhondo ya Israyeli inathawa, ndipo Benjamini anayamba kuwakantha ndi kuwagwaza amuna a Israyeli, ngati amuna makumi atatu, pakuti anati, Ndithu Tawakantha konse pamaso pathu, monga ku nkhondo yoyambayo.
40. Koma pamene mtambo unayamba kukwera m'mudzi ngati utsi uti tolo, Abenjamini anaceuka, ndipo taonani, pamodzi ponse panafuka utsi kumwamba.
41. Natembenuka amuna a Israyeli; nadabwa amuna a Benjamini; popeza anaona kuti cidawagwera coipa.
42. Nabwerera iwo pamaso pa amuna a Israyeli kumka njira ya cipululu; koma nkhondo inawaloodetsa; ndi aja oturuka m'mudzi anawaononga pakati pao.
43. Anawazinga Abenjamini, anawapitikitsa, nawapondereza pampumulo mpaka pandunji pa Gibeya, koturukira dzuwa.
44. Ndipo adagwa a Benjamini amuna zikwi khumi ndi zisanu ndi zitatu; iwo onse ndiwo ngwazi.
45. Natembenuka iwo, nathawira kucipululu ku thanthwe la Rimoni; koma anawakunkha m'makwalala amuna zikwi zisanu; nawalondetsa ku Gidomu, nakantha a iwowa amuna zikwi ziwiri.
46. Potero onse amene adagwa a Benjamini tsiku lija, ndiwo amuna zikwi makumi awiri mphambu zisanu, akusolola lupanga; iwo onse ndiwo ngwazi.
47. Koma amuna mazana asanu ndi limodzi anabwerera nathawira kucipululu, ku thanthwe la Rimoni, nakhala m'thanthwe la Rimoni miyezi inai.