Ndipo Yehova anakantha Benjamini pamaso pa Israyeli; ndi ana a Israyeli anawaononga a Benjamini tsiku lija amuna zikwi makumi awiri ndi zisanu, kudza zana limodzi; awa onse ndiwo akusolola lupanga.