22. Koma anthu, ndiwo amuna a Israyeli, anadzilimbitsa nanikanso nkhondo kumene anandandalika tsiku loyambalo.
23. Ndipo ana a Israyeli anakwera nalira misozi pamaso pa Yehova mpaka madzulo; nafunsira kwa Yehova ndi kuti, Ndiyandikizenso kodi kulimbana nkhondo ndi ana a Benjamini mbale wanga? Ndipo Yehova anati, Mumkwerere.
24. Potero ana a Israyeli anayandikira ana a Benjamini m'mawa mwace.
25. Ndipo Benjamini anawaturukira ku Gibeya m'mawa mwace, naononganso a ana a Israyeli amuna zikwi khumi ndi zisanu ndi zitatu kuwagoneka pansi; ndiwo onse osolola lupanga.
26. Pamenepo ana onse a Israyeli ndi anthu onse anakwera nafika ku Beteli, nalira misozi, nakhala pansi pomwepo pamaso pa Yehova, nasala cakudya tsiku lomwelo mpaka madzulo; napereka nsembe zopsereza ndi nsembe zoyamika pamaso pa Yehova.
27. Ndipo ana a Israyeli anafunsira kwa Yehova; pakuti likasa la cipangano la Mulungu linakhala komweko masiku aja,
28. namaima ku likasalo Pinehasi mwana wa Eleazare mwana wa Aroni, masiku aja; nati, Kodi nditurukenso kulimbana nkhondo ndi ana a Benjamini mbale wanga, kapena ndileke Ndipo Yehova anati, Kwerani, pakuti mawa ndidzampereka m'dzanja lako.
29. Ndipo Israyeli anaika olalira Gibeya pozungulira pace.
30. Ndipo ana a Israyeli anakwerera ana a Benjamini tsiku lacitatu, na nika pa Gibeya monga nthawi zina.
31. Naturuka ana a Benjamini kukomana ndi anthuwo, nakokedwa kutali ndi mudzi, nayamba kuwakantha ndi kuwapha anthu amuna a Israyeli, ngati makumi atatu monga nthawi zina, m'makwalala, limodzi la awo lokwera kumka ku Beteli, ndi lina ku Gibeya kuthengo.
32. Ndipo ana a Benjamini anati, Tawakantha pamaso pathu monga poyamba paja. Koma ana a Israyeli anati, Tithawe, tiwakokere kutari ndi mudzi kumakwalala.
33. Nauka amuna onse a Israyeli m'malo ao nanika ku Baalatamari; naturuka Aisrayeli olalira aja m'malo mwao, m'Maare-geba.
34. Ndipo anadza pandunji pa Gibeya amuna osankhika m'Israyeli monse zikwi khumi, nikula nkhondo; koma sanadziwa kuti coipa ciri pafupi kuwakhudza.
35. Ndipo Yehova anakantha Benjamini pamaso pa Israyeli; ndi ana a Israyeli anawaononga a Benjamini tsiku lija amuna zikwi makumi awiri ndi zisanu, kudza zana limodzi; awa onse ndiwo akusolola lupanga.