1. Pamenepo anaturuka ana onse a Israyeli, nuunjikana msonkhano kwa Yehova ku Mizipa ngati munthu mmodzi, kuyambira ku Dani mpaka Beereseba ndi dziko la Gileadi lomwe.
2. Ndipo akuru a anthu onse a mapfuko onse a Israyeli anadziimika mu msonkhano wa anthu a Mulungu, anthu oyenda pansi zikwi mazana anai akusolola lupanga,
3. Ndipo ana a Benjamini anamva kuti ana a Israyeli adakwera kumka ku Mizipa, Nati ana a Israyeli, Nenani, coipa ici cinacitika bwanji?