Oweruza 19:29-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

29. Ndipo pofika iye kunyumba kwace, anatenga mpeni, nagwira mkazi wace wamng'onoyo namgawa ciwalo ciwalo magawo khumi ndi awiri, namtumiza ku mame onse a Israyeli.

30. Ndipo kunali kuti onse amene anaciona anati, Sicinacitika, inde sicinaoneka cotere ciyambire tsiku lokwera ana a Israyeli kuturuka m'dziko la Aigupto mpaka lero lino; lingiriranipo, mupangane nzeru, nimunene.

Oweruza 19