28. Koma mfumu ya ana a Amoni sanamvera mau a Yefita anamtumizirawo.
29. Pamenepo mzimu wa Yehova unamdzera Yefita, napitira iye ku Gileadi, ndi Manase, napitira ku Mizipa wa Gileadi, ndi kucokera ku Mizipa wa Gileadi anapitira kwa ana a Amoni.
30. Ndipo Yefita anawindira Yehova cowinda, nati, Mukaperekatu ana a Amoni m'dzanja langa, ndipo kudzali kuti ciri conse cakuturuka pakhomo pa nyumba yanga kudzakomana nane pakubweranso ine ndi mtendere kucokera kwa ana a Amoni, cidzakhala ca Yehova, ndipo ndidzacipereka nsembe yopsereza.
32. Potero Yefita anapita kwa ana a Amoni kuwathira nkhondo; ndipo Yehova anawapereka m'dzanja lace;