Miyambi 3 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

Malangizo a kuopa, kukhulupira, ndi kumvera Yehova

1. Mwananga, usaiwale malamulo anga,Mtima wako usunge malangizo anga;

2. Pakuti adzakuonjezera masiku ambiri,Ndi zaka za moyo ndi mtendere.

3. Cifundo ndi coonadi zisakusiye;Uzimange pakhosi pako;Uzilembe pamtima pako;

4. Motero udzapezakisomo ndi nzeru yabwino,Pamaso pa Mulungu ndi anthu.

5. Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse,Osacirikizika pa luntha lako;

6. Umlemekeze m'njira zako zonse,Ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.

7. Usadziyese wekha wanzeru;Opa Yehova, nupatuke pazoipa;

8. Mitsempha yako idzalandirapo moyo,Ndi mafupa ako uwisi.

9. Lemekeza Yehova ndi cuma cako,Ndi zinthu zako zonse zoyambirira kuca;

10. Motero nkhokwe zako zidzangoti the,Mbiya zako zidzasefuka vinyo.

11. Mwananga, usapeputse mwambo wa Yehova,Ngakhale kutopa ndi kudzudzula kwace;

12. Pakuti Yehova adzudzula omwe awakonda;Monga atate mwana amene akondwera naye.

Phindu la Nzeru

13. Wodala ndi wopeza nzeru,Ndi woona luntha;

14. Pakuti malonda a nzeru aposa malonda a siliva,Phindu lace liposa golidi woyengeka.

15. Mtengo wace uposa ngale;Ndipo zonse zikukondweretsa sizilingana naye.

16. Masiku ambiri ali m'dzanja lamanja lace;Cuma ndi ulemu m'dzanja lace lamanzere.

17. Njira zace ziri zokondweretsa,Mayendedwe ace onse ndiwo mtendere.

18. Ndiyo mtengo wa moyo wa akuigwira;Wakulumirira ngwodala.

19. Yehova anakhazika dziko ndi nzeru;Naika zamwamba ndi luntha.

20. Zakuya zinang'ambika ndi kudziwakwace;Thambo ligwetsa mame.

21. Mwananga, zisacokere ku maso ako;Sunga nzeru yeniyeni ndi kulingalira;

22. Ndipo mtima wako udzatengapo moyo,Ndi khosi lako cisomo.

23. Pompo udzayenda m'njira yako osaopa,Osapunthwa phazi lako.

24. Ukagona, sudzacita mantha;Udzagona tulo tokondweretsa.

25. Usaope zoopsya zodzidzimutsa,Ngakhale zikadza zopasula oipa;

26. Pakuti Yehova adzalimbitsa mtima wako,Nadzasunga phazi lako lingakodwe.

Malangizo ena osiyana

27. Oyenera kulandira zabwino usawamane;Pokhoza dzanja lako kuwacitira zabwino.

28. Usanene kwa mnzako, Ukabwerenso,Ndipo mawa ndidzakupatsa;Pokhala uli nako kanthu.

29. Usapangire mnzako ciwembu;Popeza akhala nawe pafupi osatekeseka.

30. Usakangane ndi munthu cabe,Ngati sanakucitira coipa,

31. Usacitire nsanje munthu waciwawa;Usasankhe njira yace iri yonse.

32. Pakuti wamphulupulu anyansa Yehova;Koma cinsinsi cace ciri ndi oongoka.

33. Mulungu atemberera za m'nyumba ya woipa;Koma adalitsa mokhalamo olungama.

34. Anyozadi akunyoza,Koma apatsa akufatsa cisomo.

35. Anzeru adzalandira ulemu colowa cao;Koma opusa adzakweza manyazi.