Miyambi 24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Usacitire nsanje anthu oipa, Ngakhale kufuna kukhala nao;

2. Pakuti mtima wao ulingalira za cionongeko;Milomo yao ilankhula za mphulupulu.

3. Nzeru imangitsa nyumba;Luntha liikhazikitsa.

4. Kudziwa kudzaza zipinda zaceNdi cuma conse cofunika ca mtengo wace.

5. Mwamuna wanzeru ngwamphamvu;Munthu wodziwa ankabe nalimba.

6. Pakuti udzaponya nkhondo yako ndi upo,Ndi kupulumuka pocuruka aphungu,

7. Nzeru itarikira citsiru;Satsegula pakamwa kubwalo.

8. Wolingalira zakucita zoipaAnthu adzamcha waciwembu.

9. Maganizo opusa ndiwo cimo;Wonyoza anyansa anthu.

10. Ukalefuka tsiku la tsokaMphamvu yako icepa.

11. Omwe atengedwa kuti akafe, uwapulumutse;Omwe ati aphedwe, usaleke kuwalanditsa.

12. Ukanena, Taonani, sitinadziwa cimeneci;Kodi woyesa mitima sacizindikira ici?Ndi wosunga moyo wako kodi sacidziwa?Ndipo kodi sabwezera munthu yense monga mwa macitidwe ace?

13. Mwananga, idya uci pakuti ngwabwino,Ndi cisa cace citsekemera m'kamwamwako;

14. Potero udzadziwa kuti nzeru iri yotero m'moyo wako;Ngati waipeza padzakhala mphotho,Ndipo ciyembekezo cako sicidzalephereka.

15. Usabisalire, woipa iwe, pomanga wolungama;Usapasule popuma iyepo.

16. Pakuti wolungama amagwa kasanu ndi kawiri, nanyamukanso;Koma oipa akhumudwa pomfikira tsoka.

17. Usakondwere pakugwa mdani wako;Mtima wako usasekere pokhumudwa iye;

18. Kuti Yehova angaone kukondwa kwako, ndi kukuyesa koipa,Ndi kuleka kumkwiyira.

19. Usabvutike mtima cifukwa ca ocita zoipa;Ngakhale kucitira nsanje amphulupulu;

20. Pakuti woipayo sadzalandira mphotho;Nyali ya amphulupulu idzazima.

21. Mwananga, opa Yehova ndi mfumu yomwe,Osadudukira anthu osinthasintha.

22. Pakuti tsoka lao lidzaoneka modzidzimuka;Ndipo ndani adziwa cionongeko ca zaka zao?

23. Izinso ziri za anzeru.Poweruza cetera siliri labwino.

24. Wonenakwa woipa, Wolungama iwe;Magulu a anthu adzamtemberera, mitundu ya anthu idzamkwiyira,

25. Omwe amdzudzula adzasekera,Nadzadalitsika ndithu.

26. Wobwezera mau oongokaApsompsona milomo.

27. Longosola nchito yako panjapo, nuikonzeretu kumunda;Pambuyo pace ndi kumanga nyumba yako.

28. Usacitire mnzako umboni womtsutsa opanda cifukwa;Kodi udzanyenga ndi milomo yako?

29. Usanene, Ndidzamcitira zomwezo anandicitira ine;Ndidzabwereza munthuyo monga mwa macitidwe ace.

30. Ndinapita pa munda wa wolesi,Polima mphesa munthu wosowa nzeru.

31. Taonani, ponsepo panamera minga,Ndi kuwirirapo khwisa;Chinga lace lamiyala ndi kupasuka.

32. Pamenepo ndinayang'ana ndi kuganizira,Ndinaona ndi kulandira mwambo.

33. Tulo tapang'ono, kungoodzera pang'ono,Kungomanga manja pang'ono m'kugona,

34. Ndipo umphawi wako udzafika ngati mbala;Ndi kusauka kwako ngati munthu wacikopa.