Mateyu 5:4-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Odala ali acisoni; cifukwa adzasangalatsidwa.

5. Odala ali akufatsa; cifukwa adzalandira dziko lapansi.

6. Odala ali akumva njala ndi ludzu la cilungamo; cifukwa adzakhuta.

7. Odala ali akucitira cifundo; cifukwa adzalandira cifundo.

8. Odala ali oyera mtima; cifukwa adzaona Mulungu.

9. Odala ali akucita mtendere; cifukwa adzachedwa ana a Mulungu.

10. Odalaaliakuzunzidwacifukwa ca cilungamo: cifukwa uli wao Ufumu wa Kumwamba.

11. Odala muli inu m'mene adzanyazitsa inu, nadzazunza inu, nadzakunenerani monama zoipa ziri zonse cifukwa ca Ine.

12. Sekerani, sangalalani: cifukwa mphotho yanu ndi yaikuru m'Mwamba: pakuti potero anazunza aneneri anakhalawo musanabadwe inu.

13. Inu ndinu mcere wa dziko lapansi; koma mcerewo ngati uka: sukuluka, adzaukoleretsa ndi ciani? Pamenepo sungakwanirenso kanthu konse, koma kuti ukaponyedwe kunja, nupondedwe ndi anthu.

14. Inu ndinu kuunika kwa dziko lapansi. Mudzi wokhazikika pamwamba pa phiri sungathe kubisika.

15. Kapena sayatsa nyali, ndi kuibvundikira m'mbiya, koma aiika iyo pa coikapo cace; ndipo iunikira onse: ali m'nyumbamo.

16. Comweco muwalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona nchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.

17. Musaganize kuti ndinadza Ine kudzapasula cilamulo kapena ane, neri: sindinadza kupasula, koma kukwaniritsa.

18. Pakuti indetu ndinena kwa inu, Kufikira litapitirira thambo ndi dziko, kalemba kakang'ono kamodzi kapena kansonga kace kamodzi sikadzaeokera kucilamulo, kufikira zitacitidwa zonse.

19. Cifukwa cace yense wakumasula limodzi la malangizo amenewa ang'onong'ono, nadzaphunzitsa anthu comweco, adzachulidwa wamng'onong'ono mu Ufumu wa Kumwamba; koma yense wakucita ndi kuphunzitsa awa, iyeyu adzachulidwa wamkuru mu Ufumu wa Kumwamba.

20. Pakuti ndinena ndi inu, ngati cilungamo canu sicicuruka coposa ca alembi ndi Afarisi, simudzalowa konse mu Ufumu wa Kumwamba.

21. Munamva kuti kunanenedwa kwa iwo akale, Usaphe; koma yense wakupha adzakhala wopalamula mlandu:

22. koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wokwiyira mbale wace wopanda cifukwa adzakhala wopalamula mlandu; ndipo amene adzanena ndi mbale wace, Wopanda pace iwe, adzakhala wopalamula mlandu wa akuru: koma amene adzati, Citsiru iwe: adzakhala wopalamula gehena wamoto.

23. Cifukwa cace ngati ulikupereka mtulo wako pa guwa la nsembe, ndipo pomwepo ukakumbukira kuti mbale wako ali ndi kanthu pa iwe,

Mateyu 5