Mateyu 26:5-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Koma ananena iwo, Pa dzuwa la cakudya iai, kuti pasakhale phokoso la anthu.

6. Ndipo pamene Yesu anali m'Betaniya, m'nyumba ya Simoni wakhate,

7. anadza kwa Iye mkazi, anali nayo nsupa yaalabastero ndi mafuta onunkhira bwino a mtengo wapatari, nawatsanulira pamutu pace, m'mene Iye analikukhala pacakudya.

8. Koma m'mene ophunzira anaona, anada mtima, nanena, Cifukwa ninji kuononga kumeneku?

9. Pakuti mafuta awa akadagulitsa ndalama zambiri, ndi kuzipatsa anthu aumphawi.

10. Koma Yesu podziwa, anati kwa iwo, Mumbvutiranji mkaziyu? popeza andicitira Ine nchito yabwino.

11. Pakuti nthawi zonse muli nao aumphawi pamodzi nanu; koma simuli ndi Ine nthawi zonse.

12. Pakuti mkaziyo, m'mene anathira mafuta awa pathupi panga, wandicitiratu ici pa kuikidwa kwanga.

13. Indetu ndinena kwa inu, kumene kuli konse uthenga uwu wabwino udzalalikidwa m'dziko lonse lapansi, ici cimene mkaziyo anacitaci cidzakambidwanso cikumbukiro cace.

14. Pomwepo mmodzi wa khumi ndi awiriwo, dzina lace Yudase Isikariote, anamuka kwa ansembe akuru,

15. nati, Mufuna kundipatsa ciani, ndipo ine ndidzampereka Iye kwa inu? Ndipo iwo anamwerengera iye ndalama zasiliva makumi atatu.

16. Ndipo kuyambira pamenepo iye anafunafuna nthawi yabwino yakuti ampereke Iye.

17. Ndipo tsiku loyamba la mkate wopanda cotupitsa, ophunzira anadza kwa Yesu, nati, Mufuna tikakonzere kuti Paskha, kuti mukadye?

18. Nati Iye, Mukani kumzinda kwa munthu wangana, mukati kwa iye, Mphunzitsi anena. Nthawi yanga yayandikirai ndidzadya Paskha kwanu pamodzi ndi ophunzira anga.

Mateyu 26