1. Ndipo Yesu anaturuka kuKacisi; ndipo ophunzira ace anadza kudzamuonetsa cimangidwe ca Kacisiyo.
2. Koma Iye anayankha nati kwa iwo, Simuona izi zonse kodi? indetu ndinena kwa inu, Sipadzakhala pano mwala umodzi pa unzace, umene sudzagwetsedwa.
3. Ndipo pamene Iye analikukhala pansi pa phiri la Azitona, ophunzira anadza kwa Iye pa yekha, nanena, Mutiuze ife zija zidzaoneka liti? ndipo cizindikiro ca kufika kwanu nciani, ndi ca mathedwe a nthawi ya pansi pano?
4. Ndipo Yesu anayankha nati kwa iwo, Yang'anirani, asasokeretse inu munthu.
5. Pakuti ambiri adzafika m'dzina langa, nadzanena, Ine ndine Kristu, nadzasokeretsa anthu ambiri.
6. Koma inu mudzayamba kumva za nkhondo, ndi mbiri za nkhondo; onani, musadere nkhawa; pakuti kuyenera kuti izi zioneke; koma citsiriziro sicinafike.