1. Ndipo Yesu anaturuka kuKacisi; ndipo ophunzira ace anadza kudzamuonetsa cimangidwe ca Kacisiyo.
2. Koma Iye anayankha nati kwa iwo, Simuona izi zonse kodi? indetu ndinena kwa inu, Sipadzakhala pano mwala umodzi pa unzace, umene sudzagwetsedwa.
3. Ndipo pamene Iye analikukhala pansi pa phiri la Azitona, ophunzira anadza kwa Iye pa yekha, nanena, Mutiuze ife zija zidzaoneka liti? ndipo cizindikiro ca kufika kwanu nciani, ndi ca mathedwe a nthawi ya pansi pano?
4. Ndipo Yesu anayankha nati kwa iwo, Yang'anirani, asasokeretse inu munthu.
5. Pakuti ambiri adzafika m'dzina langa, nadzanena, Ine ndine Kristu, nadzasokeretsa anthu ambiri.
6. Koma inu mudzayamba kumva za nkhondo, ndi mbiri za nkhondo; onani, musadere nkhawa; pakuti kuyenera kuti izi zioneke; koma citsiriziro sicinafike.
7. Pakuti mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina; ndipo kudzakhala njala ndi zibvomezi m'malo akuti akuti.
8. Koma ndizo zonsezi zowawa zoyamba.
9. Pamenepo adzakuperekani kunsautso, nadzakuphani; ndipo anthu a mitundu yonse adzadana nanu, cifukwa ca dzina langa.
10. Ndipo pomwepo ambiri adzakhumudwa, nadzaperekana wina ndi mnzace, nadzadana wina ndi mnzace.
11. Ndipo aneneri onama ambiri adzauka, nadzasokeretsaanthuambiri.
12. Ndipo cifukwa ca kucuruka kwa kusayeruzika, cikondano ca anthu aunyinji cidzazirala.
13. Koma iye wakulimbika cilimbikire kufikira kucimariziro, yemweyo adzapulumuka.