Mateyu 21:1-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo parnene iwo anayandikira ku Yerusalemu, nafika ku Betefage, ku phiri la Azitona, pamenepo Yesu anatumiza ophunzira awiri,

2. nanena kwa iwo, Mukani ku mudzi wopenyana ndi inu, ndipo pomwepo mudzapeza buru womangidwa, ndi mwana wace pamodzi nave, masulani iwo, mudze nao kwa Ine.

3. Ndipo munthu akanena kanthu ndi inu, mudzati, Ambuye asowa iwo, Ndipo pomwepo adzawatumiza.

4. Ndipo ici cinatero, kuti cikacitidwe conenedwa ndi mneneri kuti,

5. Tauzani mwanawamkazi wa Ziyoni,Taona, Mfumu yako idza kwa iwe,Wofatsa ndi wokwera pa buru,Ndi pa kaburu, mwana wa nyama yonyarnula katundu.

6. Ndipo ophunzirawo anamuka, nacita monga Yesu anawauza;

7. nabwera ndi buru ndi mwana wace, naika pa iwo zobvala zao, nakhala Iye pamenepo.

8. Ndipo ambirimbiri a mpingowo anayala zobvala zao panjira; Ndipo ena anadula nthambi za mitengo, naziyala m'njirarno.

9. Ndipo mipingo yakumtsogolera ndi yakumtsatira, inapfuula, kuti, Hosana kwa Mwana wa Davide! Wolemekezeka ndiye wakudza m'dzina la Ambuye! Hosana m'Kumwambamwamba!

10. Ndipo m'mene adalowa m'Yerusalemu mudzi wonse unasokonezeka, nanena, ndani uyu?

11. Ndipo makamu a anthu anati, Uyu ndi mneneri Yesu wa ku Nazarete wa ku Galileya.

12. Ndipo Yesu analowa ku Kacisi wa Mulungu naturutsira kunja onse akugulitsa ndi kugula malonda, nagubuduza magome a osintha ndalama, ndi mipando ya ogulitsa nkhunda;

13. nanena kwa iwo, Calembedwa, Nyumba yanga idzanenedwa nyumba yakupemphera; koma inu mwaiyesa phanga la acifwamba.

14. Ndipo anadza kwa Iye kuKacisiko akhungu ndi opunduka miyendo, naciritsidwa.

15. Koma ansembe akuru ndi alembi, m'mene anaona zozizwitsa zomwe Iye anazicita, ndi ana alinkupfuula kuKacisiko kuti, Hosana kwa Mwana wa Davide, anapsa mtima,

16. nanena kwa Iye, Mulinkumva kodi cimene alikunena awa? Ndipo Yesu ananena kwa iwo, Inde: simunawerenga kodi, M'kamwa mwa makanda ndi oyamwa munafotokozera zolemekeza?

Mateyu 21