Mateyu 20:20-34 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Pomwepo anadza kwa Iye amace a ana a Zebedayo ndi ana ace omwe, namgwadira, ndi kumpempha kanthu.

21. Ndipo Iye anati kwa iye, Ufuna ciani? Iye ananena, Lamulirani kuti ana anga awiri amenewa adzakhale, wina ku dzanja lanu lao manja, ndi wina kulamanzere, mu ufumu wanu.

22. Koma Yesu anayankha nati, Inu simudziwa cimene mupempha, Kodi mukhoza kumwera cikho nditi ndidzamwere Ine? Iwo ananena kwa Iye, Ife tikhoza.

23. Iye ananena kwa iwo, Cikho canga mudzamweradi; koma kukhala ku dzanja lamanja kwangandi kulamanzere, sikuli kwanga kupatsa, koma kuli kwa iwo omwe kwakonzedweratu ndi Atate wanga.

24. Ndipo m'mene khurniwo anamva, anapsa mtima ndi abale awiriwo.

25. Koma Yesu anawaitana, nati, Mudziwa kuti mafumu a anthu amadziyesa okha ambuye ao, ndipo akuru ao amacita ufumu pa iwo.

26. Sikudzakhala comweco kwa inu ai; koma amene ali yense akafuna kukhala warnkuru mwa inu, adzakhala mtumiki wanu;

27. ndipo amene ali yense akafuna kukhala woyamba mwa inu, adzakhala kapolo wanu:

28. monga Mwana wa munthu sanadza kutumikiridwa koma kutumikira, ndi kupereka moyo wace dipo la anthu ambiri.

29. Ndipo pamene iwo analikuturuka m'Yeriko, khamu lalikuru la anthu linamtsata Iye.

30. Ndipo onani, anthu akhungu awiri anakhala m'rnphepete mwa njira; m'mene iwo anamva kuti Yesu analikupitirirapo, anapfuula nati, Muticitire ife cifundo, Inu Mwana wa Davide.

31. Ndipo khamulo linawaletsa, kuti atonthole: koma anakuwitsa, nanena, Ambuye, muticitire cifundo, Inu Mwana wa Davide.

32. Ndipo Yesu anaima, nawaitana, nati, Mufuna kuti ndikucitireni ciani?

33. Ananena kwa Iye, Ambuye, kuti maso athu apenye,

34. Ndipo Yesu anagwidwa ndi cifundo, nakhudza maso ao; ndipo pornwepo anapenyanso, namtsata Iye.

Mateyu 20